Kishore Kumar Hits

Maskal - Kudzagwa Mvula текст песни

Исполнитель: Maskal

альбом: Umunthu


Oooh! ooh
Yeah ooh whoo!
Onani bambo awo
Ali ndi business awo
Koma ndi mavuto kunyumba kwawo
Geni ija yalowa m'madzi
Pali m'nyamata uyu
Anavutika mkuphunzira
Lero watopa mkupilira
Kuyesetsa kupeza ntchito oh-oh-oh
Banja amkalifuna
Kuti ayambe moyo wina
Alephera kumanga umodzi
Lero kwangotsala dzina
Koma tsiku limodzi (kudzagwa mvula)
Tsiku limodzi (kudzagwa mvula)
Oooh oh-oh-oh (kudzagwa mvula)
Mvula idzabwera (idzatsuka mavuto onse)
Chaka ndi chimodzi (kudzagwa mvula)
Dzuwa ndi limodzi (kudzagwa mvula)
Hee eh-eh-eh (kudzagwa mvula)
Idzatsuka mavuto onse
Kaya matenda (mvula idzatsuka)
Kaya njala (mvula idzatsuka)
Kusowa kwa chikondi (mvula idzatsuka)
Idzatsuka mavuto onse
Oooh oh, oooh oh, oooh oh
Kudzagwa mvula!
Yeah, amati ndi wolemera
Ena amati ndi olephera
Samatopa ndi kupemphera
Kupempha kufuna mwana
Mwanayu atsala ndi ndani?
Nanga amusamale n'ndani?
Imfa inatenga mayi wake
Lero yatenga bambo
Makolo ake ali kuti mwanayu?
Matenda anatenga kuti mwanayu?
Poti akali chichepere
Gwero la matenda ake sadziwa
Koma tsiku limodzi (kudzagwa mvula)
Tsiku limodzi (kudzagwa mvula)
Oooh oh-oh-oh (kudzagwa mvula)
Mvula idzabwera (idzatsuka mavuto onse)
Chaka ndi chimodzi (kudzagwa mvula)
Dzuwa ndi limodzi (kudzagwa mvula)
Hee eh-eh-eh (kudzagwa mvula)
Idzatsuka mavuto onse
Chaka ndi chimodzi (mvula idzatsuka)
Dzuwa ndi limodzi (mvula idzatsuka)
Oooh oh-oh-oh (mvula idzatsuka)
(Mvula idzabwera) idzatsuka mavuto onse
Usataye mtima
Ngakhale kuli mdima
Pemphera molimbika
Mvula idzabwera
Kusowa kwa chikondi
Usataye mtima
Kuzuzika ndi matendawa
Chaka ndi chimodzi (kudzagwa mvula)
Dzuwa ndi limodzi (kudzagwa mvula)
Hee eh-eh-eh (kudzagwa mvula)
Idzatsuka mavuto onse
Kaya matenda (kudzagwa mvula)
Kaya njala (kudzagwa mvula)
Mvula idzatsuka (kudzagwa mvula) idzatsuka
Idzatsuka mavuto onse
Kusowa kwa chikondi (mvula idzatsuka)
Kaya njala (mvula idzatsuka)
Hee yah-yah-yah (mvula idzatsuka)
(Idzatsuka mavuto onse)

Поcмотреть все песни артиста

Другие альбомы исполнителя

Похожие исполнители