Kalekale ndili wang'ono
Agogo anandiuza nthano
Nthano yomvetsa chisoni
Nanunso muyimve khalani
Ananyamata pachibale atatu
Anali pa ulendo
Wokafuna ntchito kutali
Panjira anatola chikwama
Ayang'ane mkati mwa chikwama mo
Munali dzi ndalama mapeto
Atapumila ulendo wawo
Anatuma wang'ono pa onse
Tapita ukaguke fanta
Uyo munapangana apobe
Nayenso anakonza chiwembu
Adathira takemi mu fanta ooh
Ndi ndani wadyela?
Adakumana okha-okha adyela
Mapeto ake adatola wodutsa chikwana
Ifenso lero
Takumana okha-okha adyela
Iwe ndi ine
Akulemera wobwera amwenye
Ah umvetse
Mphwanga umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
Umvetse, wadyela umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
♪
Zokhazokha zioneka leroli
Anthufe chikutisawutsa
Ndi mtima wosafuna
Kugawana zomwe tapata
Tachulutsa kuwalirana
Komanso kupikisana
Komatu mapeto ake
Zonsezi woluza ndife
Bread akakwera mtengo
M'malo mogwirizana kukamba
Popeza ena amatama
Akagula ma loaf asanu
Kukanika kugwirizana
Alolera kuti mowa usapse
Kusiyana ndikuti agawane
Ndalama ndiwe nayela ooh
Ndi ndani wadyela?
Adakumana okha-okha adyela
Mapeto ake adatola wodutsa chikwana
Ifenso lero
Takumana okha-okha adyela
Iwe ndi ine
Akulemera wobwera amwenye
Ah umvetse
Mphwanga umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
Umvetse mve-mve-mve umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
♪
Chinthu china chiwononga ubwenzi
Ndi kasamalidwe ka ndalama
M'maziwononga udyo
Zidatha kumagawira
Ndalamayo muyimwele mowa
Mukaledzela muzipatsa mahule
Pomwepo mupeze chamba
Za nyumba mudzagula liti?
Amayi wanu munawalonjeza
Mukalemera ndidzakuthandizani
Lero mungomwa mowa
Mpaka kugona mdzimbudzi
Ndayipa poti lero zayenda
Simufuna kuti tigawane
Komatu mapeto ake
Adzawina wodutsa kunjira ooh
Ndi ndani wadyela?
Adakumana okha-okha adyela
Mapeto ake adatola wodutsa chikwana
Ifenso lero
Takumana okha-okha adyela
Iwe ndi ine
Akulemera wobwera amwenye
Iwe umvetse
Mphwanga umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
Umvetse, boy umvetse iwe
Umvetse iwe
Adatola wodutsa chikwama
Umvetse, mphwanga umvetse iwe
Umvetse, adatola wodutsa chikwama
Поcмотреть все песни артиста
Другие альбомы исполнителя