Ine ndikhumba, Mbuye Yesu
Mudzakhale pompo mkamadzafa
Ndikamasimba za imfa yanga
Abwenzi ambiri samakondwa
Koma ndithu tonsefe tidzafa
Ngati si mawa mwina mkuja
Ine nditi pa maliro anga
Msadzachulutse kundiyamika
Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti)
Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi)
Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe)
Wana amayi amasiye (zawo alandire)
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi
Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe
Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito
Abale anga osawuka-wa mukawaganizira
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Musadzagule bokosi lodula
Musadzatchule zakutchuka kwanga
Musadzanene za chuma changa
Musadzanene za nzeru zanga
Ngati mudzafune kunena kanthu
Mudzati ndidayesetsa kumenya
Kumenya nkhondo yabwino
Ndinali soldier kwa amphawi
Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti)
Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi)
Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe)
Wana amayi amasiye (zawo alandire)
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi
Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe
Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito
Abale anga osawuka-wa mukawaganizira
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Aah ooh
♪
Abwenzi anga sanali achuma
Anali olema ndi amphawi
Andende olira mdzipatala
Iih amayi amasiye
Musadzayiwale ndinayesetsa
Kukonda mtundu wa munthu
Mtembo wanga msawutaye ntchire
Ana a mawa adzakumbuke
Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti)
Odwala athandizidwa (mwachangu ndi chikondi)
Pa anthenda aweluzidwa (asanamangidwe)
Wana amayi amasiye (zawo alandire)
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi
Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe
Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito
Abale anga osawuka-wa mukawaganizira
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wangawu udzagona
♪
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Wana amphawi ndi wolemera aphunzire zimodzi
Ngakhale wolemera akalakwa amangidwe
Olumara ndi akhungu alembedweso ntchito
Abale anga osawuka-wa mukawaganizira
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Marley udzagona
Nzimu wa Toshi udzagona
Nzimu wa Etsi udzagona
Nzimu wa Luther udzagona
Nzimu wa Ghandi udzagona
Nzimu wa Chirwa udzagona
(Nzimu wa Yesu udzagona)
Поcмотреть все песни артиста
Другие альбомы исполнителя