Kishore Kumar Hits

Lucius Banda - Mmodzi Wovuta текст песни

Исполнитель: Lucius Banda

альбом: Yahwe


Mwana iwe umandidabwitsa
Kodi kwanu kuja udatenga ndani iwe?
Bambo ako ndi munthu wofatsa
Amayi ako kutchalitchi ngamvano
Azimphwako mmabwana nzintchito
Mulungo wako akuwulutsa ndege
Akulu anati mimba ndi nchipala
Chipala cha iwe ah toto

Mwana iwe zomwe ukuchita
Ndi zachilendo kwa tonse nzoopsa
Makolo ako ngachuma kwambiri
Nchifukwa chani ukumka mumawa?
Mkazi wako ngokongola zedi
Ulimbanaso ndi edzi pa Lunzu
Kumangopezeka malo otchuka
Kupasiya uku Lejest ku Bwandilo ooh
Banja lililonse anzanga
Simulephera wovutitsa m'modzi
Olo muchipani chimene
Simulephera wopenga angapo
Ndi udindo wathu ife abwinofe
Kutsogolera panjira yabwino
Pakuti ngati umenyana mchitsiru
Anthu owona sangalekanitse

Pamene mwana wina atchukitsa dzina
La bambo ake ndi mbiri yabwino
Banja lomwelo mutuluka wina
Wotukwanitsa makolo ndi kuba
Pamene atsogoleri ena atangandidwa
Kukonza nsewu, milatho, sukulu
Phungu wina ali otanganidwa
Akugulitsa rest house yake oh iih

Amphaka ndi agalu asiya ndewu
Akuwonera chi ndewu cha anthu
Pamene akhristu akunja ali kuyesetsa
Kutumizira amphawi dzovala
Katundu uja akafika kuno
Amangopita kwa akazi azibwenzi
M'malo mogwira ntchito yake ya ubusa
Atuma wena iye ali ndi akazi
Banja lililonse anzanga
Simulephera wovutitsa m'modzi
Olo muchipani chimene
Simulephera wopenga angapo
Ndi udindo wathu ife abwinofe
Kutsogolera panjira yabwino
Pakuti ngati umenyana ndi chitsiru
Anthu owona sangalekanitse

Ih yah oooh
Mwana wanga iwe!
Rastafari

Banja lililonse anzanga
Simulephera wovutitsa m'modzi
Olo mchipani chimene
Simulephera wosimbwa angapo
Ndi udindo wathu ife abwinofe
Kutsogolera panjira yabwino
(Pakuti ngati umenyana mchitsiru)
(Anthu owona sangalekanitse)

Поcмотреть все песни артиста

Другие альбомы исполнителя

Life

2016 · альбом

Time

2013 · альбом

Похожие исполнители

Lawi

Исполнитель

Ritaa

Исполнитель