Angoni ndikakwatira, muzandiphere chikonze
Mzatchinjireze uwende, muzautsire tsabola
Oh angoni oh angoni
Kuti chingoni chikondwe
Msazalephere kabiya
Lawi lawi ukuwira
Nkachipanda wa masese
Oh angoni oh angoni
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodya zawo ndizinai
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodyazathu ndizinai
Nyama, mowa, ng'oma, kamkazi kali pa mbalipo
Koimba nthungululu
Paukwati wanga abale
Msakanditengere band
Mkandimemezere ng'oma ya chikuse wa Gomani
Oh angoni oh angoni
No zovala aNgoni
Msavutike ndi masuit
Mkaziwanga veil ayi
Tikonzereni zibiya
Oh aNgoni oh aNgoni
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodya zawo ndizinai
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodyazathu ndizinai
Nyama, mowa, ng'oma, kamkazi kali pa mbalipo
Koimba nthungululu
Angoni amandiwaza
Savutika ndizambiri
Mphalabungu nkhale mbewa
Chinkhumba ndiye nyamayo
Oh aNgoni OH aNgoni
Kuti mudziwe ndingoni
Mzaonere chikhalidwe
Samakonda zachibwana
Zandewu samakaika
Oh angoni oh angoni
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodya zawo ndizinai
Ngodya za angoni nzingati?
Ngodyazathu ndizinai
Nyama, mowa, ng'oma, kamkazi kali pa mbalipo
Koimba nthungululu
Поcмотреть все песни артиста
Другие альбомы исполнителя